Kucheza komwe kwachitika mwezi wa July/August 2024
Zikomo kwambiri potenga nawo mbali mukucheza ndi anthu komwe ife tinachita limodzi ndi anzathu ena omwe tikupanga nawo kafukufuku muno m’Malawi. M’musimu muli uthenga wina okhudza kafukufukuyu.
Akugwiritsa ntchito kafukufukuyu ndani?
A Opportunity International (OI) muno m’Malawi atipempha kuti tichite kafukufukuyu ndi kuunikira momwe pologalamu yawo yotchedwa ‘’Kulimbikitsa Ndondomeko Zachuma m’Madera Akumidzi muno m’Malawi‘’ yomwe cholinga chake ndikupititsa patsogolo katundu ndi zithandizo za makono zomwe zimaperekedwa kwa alimi ndi mwayi wa maphunziro a zachuma ndi katundu yakhudzira anthu.
Chifukwa chani panafunikira kuti acheze nafe?
A Opportunity International atipempha kuti tiyankhulane ndi alimi omwe akukhudzidwa ndi pologalamuyi pofuna kudziwa za kusintha kwina kulikonse pa miyiyo yawo mu zaka zitatu zapitazi. Anthu ochita kafukufuku ochokera ku bungwe la PALM Consulting Limited la kuno ku Malawi akugwira ntchito m’malo mwa a Bath Social and Development Research, yomwe ndi kampani ya kafukufuku yoyima payokha yaku UK. Munasankhidwa kuti mutenge nawo mbali mu kafukufukuyu kuti ife timve za zomwe mwakumana nazo/zomwe mwadutsamo ndi zomwe mukuganiza kuti ndi zinthu zofunikira kwambiri pa kayendetsedwe ka ulimi wanu.
Anthu okwana 70 ndi omwe anafunsidwa mafunso, 10 anali abambo komanso 60 anali amayi. Kugawa kotereku kunachitika chifukwa OI inali ndi chidwi pa kutengapo gawo kwa amayi pa nkhani zachuma.
Kucheza ndi anthu payekha payekha kuchitikira m’maboma awa:
- Mulanje
- Zomba
- Dedza
- Nkhotakota
Chifukwa chani simunandiuze zokhudza polojekiti?
Tingakonde kumva zonse zomwe mukufuna kutiuza, kusiyana ndikuti mungotiuza zokhudza thandizo lomwe a Opportunity International akupereka. Tili ndi chikhulupiliro kuti kafukufukuyu athandiza omwe akupereka thandizo la zachuma ndi anthu omwe akuyendetsa polojeti kuphunzira zambiri pa zomwe zimayenda ndi zomwe sizimayenda ndi kukonza kuti zidzakhale bwino mtsogolo. Ngati pali zina zomwe mukufuna kuti tigawane, chonde lumikizanani nafe pogwiritsa ntchito makina a intaneti pa www.bathsdr.org ngati mukufuna kudziwa zambiri za momwe timagwilira ntchito.
Findings /Zomwe titapeze
Kafukufukuyu anapeza kuti kapezedwe ka ngongole kuchokera m’ma banki mkhonde komanso kugwiritsa ntchito njira za ulimi wamakono zinathandizira kukolora zochuluka, kupeza ndalama zochuluka, komanso kupeza chakudya chokwanira. Koma anthu ambiri ananena kuti nyengo yoyipa inachepetsa zokolora zawo komanso kuchepetsa ndalama zimene amapeza zomwe zinapangitsa kuti asakhale osazidalira komanso kukhala ndi chakudya chosakwanira. Nyengo yoipa makamaka inakhudza ku Zomba ndi Mulanje.
Ntchito za ulimi ndi chakudya chokwanira
Kupitilira theka la omwe anayankha mafunso ananena kuti zokolora zawo zachepa mnyengo ya posachedwapa, komanso munthu m’modzi mwa anthu atatu aliwonse ananena za kuonjezereka pamene ena ochepa ananena kuti panalibe kusintha kulikonse. Zifukwa zomwe zinathandizira kuchulukitsa zokolora zikuphatikizapo nzeru zatsopano zokhudza machitidwe amakono, kapezedwe ka zipangizo zaulimi monga feteleza ndi mbewu. Nzeru za tsopanozi zinachokera ku uphungu wa anthu ena kapena mabungwe osayimira boma.
Tikukonza zodzala chimanga chimodzichimodzi pa phando ndikuyamba kupanga mizere yaying’ono m’munda mwathu. Tinamva za njira ziwiri zimenezi kuchokera pa wailesi komanso kwa anzathu.”
Mzimayi waku Mulanje
Kusintha komwe kunatchulidwa mowirikiza kokhudza ulima kunali:
- Kulima mbeu yachilendo/ mtundu wachilendo wa mbewu.
- Kuchepetsa chiwerengero cha mbeu yomwe imadzalidwa pa phando limodzi.
- Kugwiritsa ntchito manyowa ndi feteleza ochuluka.
- Kupititsa patsogolo ulimi othilira popanga mizère pakati pa mapando
Ngakhale panali kugwiritsa ntchito njira zaulimi zamakono, anthu ena sanaonepo kusintha kulikonse pa mbeu zawo chifukwa cha nyengo yoipa monga namondwe wa Freddy,ng’amba ndi kusefukira kwa madzi. Izi zinasokoneza kwambiri alimi aku Mulanje ndi Zomba kuposa madera ena akafukufuku. Kukwera mtengo kwa zipangizo zina zofunikira paulimi ngati feteleza, mankhwala, mbeu komanso malo zinatchulidwanso mowirikiza ngati zina mwa zovuta.
Ndalama
Anthu oyankha mafunso anatiuza nkhani zabwino ndi zoipa zokhudza kusintha kwa kapezedwe ka ndalama zawo. Anthu ambiri ndalama zawo zimadalira kuchita bwino kwa mbeu zawo, ngakhale enanso ambiri amachita mabizinesi ena osakhudzana ndi ulimi komanso ganyu.
Kubwereka ndalama kuchokera kuma banki mkhonde ndi mabungwe ena obwereketsa ndalama monga FINCA kwapangitsa alimi ambiri kukhala ndi ma bizinesi oti akuyenda kapena kuyambitsa ma bizinesi a tsopano. Kusunga ndalama pogwiritsa ntchito ngongole kwathandiza alimi kupeza phindu lochuluka kuchokera m’mabizinesi awo. , kupereka mwayi kuti akulitse ma buzinesi awo. Alimi anali ndi kuthekera kochuluka kosunga ndalama , kugula katundu ndi kulowa magulu a banki mkhonde ngati awona kuti ali ndi ndalalam zochuluka zokapereka ku banki mkhonde ndi kubwenza ngongole.
Mzimayi waku Nkhotakota
Chaka chatha pomwe ndinaona kuti bizinesi yanga ya tomato siyimayenda ndinabwereka ndalama kuti ndiwonjezere mpamba. Ndinabwereka K500,000 kuchokera ku FINCA yomwe inali ndalama yochuluka kwambiri yomwe ndinabwerekapo kufananitsa ndi zaka zitatu zapitatzi. Bizinesi inayamba kuchita bwino nditawonjezeramo mbali ina ya ndalamazo.Izi zinachepetsa nkhawa zanga chifukwa ndinali ndi mantha kuti bizinesi yanga igwa.
Ma membala a banki mkhonde ananena kuti mwayi osunga ndi kubwereka ndalama kudzera m’magulu kunapititsa patsogolo kapezedwe kawo ka chakudya ndi kuthana ndi mavuto a zachuma. Koma, anthu omwe anali ndi ndalama zochepa ananena kuti samafuna kubwereka ndalama m’magulu chifukwa anali ndi mantha ndi ndondomeko za kabwezedwe ka ngongole. Anthu enanso amagwa mphwayi chifukwa chosagawana mwachilungamo ndalama m’magulu. Kugwiritsa ntchito chithandizo cha ma banki kudzela m’magulu amenewa kunali kochepa. Ma banki anapereka mwayi kumagulu kuti atha kubwereka ndalama zochulukirapo koma anthu ena anaopa ndondomeko ya kabwezedwe ka ngongole.
Ziganizo za pakhomo
Azimayi ena ananena kuti anali ndi gawo lalikulu popanga ziganizo zokhudza ndalama kuyambira pomwe analowa mu banki mkhonde, komwe amayendetsa ndalama zosonkha pawokha kapena potsatira kukambirana ndi amuna awo. Kwa azimayi ambiri, ndalama zochokera ku mabizinesi awo zinathandiza kupititsa patsogolo kuzidalira pa zachuma komanso kupanga ziganizo pawokha.
Kukhala membala wa banki mkhonde kwanditsegula maso kuti ndikhoza kukhala ndi mphamvua yopanga chiganizo pa ndalama zomwe ndimapanga m’malo mowasiyira amuna anga.
Mzimayi waku Mulanje
Ungwiro ndi chiyembekezo chabwino cha mtsogolo
Panali kugawikana pa mayankho okhudza kusintha pa ungwiro, kupilira pa mavuto a zachuma ndi chiyembekezo cha mtsogolo, makamaka mavuto okhudza ulimi chifukwa cha nyengo. Pafupifupi theka la anthu oyankha mafunso(anthu 34 mwa anthu 72) anayankha kuti ungwiro wawo walowa pansi mzaka zitatu zapitazi.
Ambiri mwa oyankha mafunso anali ndi chiyembekezo chabwino chokhudza tsogolo Akukhulupilira kuti ndi ndondomeko za malimidwe zatsopano ndi njira zotsogola zopezera zipangizo za ulimi, kwa ena, kudzela mu ngongole, zidzathandiza kukolora zambiri chaka chamawa ngati nyengo ingadzakhale yabwino.
Lumikizanani nafe:
Ngati mukufuna kuwauza a Bath zambiri, kutiuza za momwe ochita kafukufuku agwilira ntchito kapena ngati muli ndi nkhawa, lembani kalata pa intaneti ku: info@bathsdr.org
Ngati pali mafunso kapena nkhawa zilizonse, ayimbireni Dr Peter Mvula omwe akutsogolera kafukufukuyu pa nambala iyi: [+265888827933/999958020]
Zikomo!