Zikomo potenga nawo mbali mukucheza kwathu komwe tinachititsa posachedwa ndi ena omwe tikuchita nawo kafukufuku muno m’Malawi.
Chifukwa chani simunandiuze dzina la pologalamu?
Nthawi zambiri sitimanena chilichonse kwa opanga kafukufuku kapena kwainu ndicholinga chokuti timve zonse zomwe mukufuna kutiuza, kusiyana ndikuti inu mungotiuza zinthu zokhudza polojekiti. Chidwi chathu chili pa zomwe inu mukuganiza kuti ndizofunika kwambiri ndipo izi zitha kukhala zokhuza zinthu zambiri kuposa za pologalamu. Izi zikutanthauza kuti ndi anthu ochita kafukufuku omwe sakudziwa za pologalamuyi!
Tili ndi chidwi kuti timve zomwe mukuganiza kuti zasintha komanso zifukwa zake, pa malimidwe anu ndi pa moyo wanu wa tsiku ndi tsiku kuphatikizapo umoyo ndi kapezedwe kanu ndi banja lanu. Tikufuna timvetsetse ngati pulojekitiyi yakhala ndi zotsatira zabwino kapena zoipa kwa alimi a mdera lino ndicholinga choti omwe amapereka thandizo la zachuma athe kuphunzirapo zambiri pa zomwe zili zabwino ndikuti mtsogolomo azipititse patsogolo.
Onani tsamba ili ngati mukufuna kudziwa zambiri za momwe timapangira kafukufuku wathu.
Zomwe titapeze
Tizalemba pano mwachidule zomwe titapeze kafukufukuyu akazatha – izi zikhoza kutenga miyezi isanu ndi umodzi (6).